Хайлт хийх үг

Genesis 1

1PACIYAMBI Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi. 2Dziko lapansi ndipo linali lopanda kanthu; ndipo mdima unali pamwamba pa nyanja; ndipo mzimu wa Mulungu unaliokufungatira pamwamba pa madzi. 3Ndipo anati Mulungu, Kuyere; ndipo kunayera. 4Ndipo anaona Mulungu kuti kuyerako kunali kwabino: ndipo Mulungu analekanitsa kuyera ndi mdima. 5Ndipo Mulungu anacha kuyerako Usana, ndi mdimawo anaucha Usiku. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku loyamba.

6Ndipo anati Mulungu, Pakhale thambo pakati pa madzi, lilekanitse madzi ndi madzi. 7Ndipo Mulungu anapanga thambo, nalekanitsa madzi anali pansi pa thambolo ndi madzi analf pamwamba pa thambolo: ndipo kunatero. 8Ndipo Mulungu analicha thambolo Kumwamba. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku laciwiri.

9Ndipo anati Mulungu, Madzi a pansi pa kumwamba asonkhane pamodzi pa malo amodzi, uoneke mtunda: ndipo kunatero. 10Ndipo Mulungu adaucha mtundawo Dziko lapansi; kusonkhana kwa madziko ndipo adaucha Nyanja: ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino. 11Mulungu ndipo anati, Dziko lapansi limere maudzu, therere lobala mbeu, ndi mtengo wazipatso wakubala zipatso monga mwa mtundu wace, momwemo muli mbeu yace, pa dziko lapansi: ndipo kunatero. 12Ndipo dziko lapansi linamera maudzu, therere lobala mbeu monga mwa mtundu wace, ndi mtengo wakubala zipatso, momwemo muli mbeu yace, monga mwa mtundu wace; ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino. 13Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lacitatu.

14Ndipo Mulungu anati, Pakhale zounikira pa thambo la kumwamba, zakulekanitsa usana ndi usiku; zikhale zizindikiro ndi nyengo, ndi masiku, ndi zaka; 15zikhale zounikira m'thambo la kumwamba, kuti ziunikire pa dziko lapansi; ndipo kunatero. 16Ndipo Mulungu anapanga zounikira zazikuru ziwiri; counikira cacikuru cakulamulira usana, counikira cacing'ono cakulamulira usiku, ndi nyenyezi zomwe. 17Mulungu ndipo adaika zimenezo m'thambo la kumwamba, kuti ziunikire pa dziko lapansi, 18nizilamulire usana ndi usiku, nizilekanitse kuyera ndi mdima: ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabino. 19Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lacinai.

20Ndipo anati Mulungu, Madzi abale zocuruka zamoyo zoyendayenda, ndi mbalame ziuluke pamwamba pa dziko lapansi ndi pamlengalenga. 21Mulungu ndipo adalenga zinsomba zazikuru ndi zoyendayenda zamoyo zakucuruka m'madzi mwa mitundu yao, ndi mbalame zamapiko, yonse monga mwa mtundu wace: ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino. 22Mulungu ndipo anadalitsa zimenezo, nati, Zibalane, zicuruke, zidzaze madzi a m'nyanja, ndi mbalame zicuruke pa dziko lapansi. 23Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lacisanu.

24Ndipo adati Mulungu, Dziko lapansi libale zamoyo monga mwa mitundu yao, ng'ombe, ndi zokwawa, ndi zinyama za dziko lapansi monga mwa mitundu yao: ndipo kunatero. 25Ndipo Mulungu anapanga zinyama za dziko lapansi monga mwa mitundu yao; ndi ng'ombe monga mwa mtundu wace, ndi zonse zakukwawa pansi monga mwa mitundu yao; ndipo Mulungu anaona kuti kunali kwabwino.

Kulengedwa kwa munthu

26Ndipo anati Mulungu, Tipange munthu m'cifanizo cathu, monga mwa cikhalidwe cathu: alamulire pa nsomba za m'nyanja, ndi pa mbalame za m'mlengalenga, ndi pa ng'ombe, ndi pa dziko lonse lapansi, ndi pa zokwawa zonse zakukwawa pa dziko lapansi. 27Mulungu ndipo adalenga munthu m'cifanizo cace, m'cifanizo ca Mulungu adamlenga iye; adalenga iwo mwamuna ndi mkazi. 28Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, mucuruke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pa nsomba za m'nyanja, ndi pa mbalame za m'mlengalenga, ndi pa zamoyo zonse zakukwawa pa dziko lapansi. 29Ndipo anati Mulungu, Taonani, ndakupatsani inu therere lonse lakubala mbeu liri pa dziko lapansi, ndi mitengo yonse m'mene muli cipatso ca mtengo wakubala mbeu; cidzakhala cakudya ca inu: 30ndiponso ndapatsa zinyama zonse za dziko lapansi, ndi mbalame zonse za m'mlengalenga, ndi zakukwawa zonse za dziko lapansi m'mene muli moyo, therere laliwisi lonse likhale cakudya: ndipo kunatero. 31Ndipo anaziona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, taonani, zinali zabwino ndithu. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lacisanu ndi cimodzi.

Buku Lopatulika 1992

©The Bible Society of Malawi, 1992

More Info | Version Index